18 Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati, 19 "Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera."
20 Petro anayankha kuti, "Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama!