Pular para o conteúdo
Publicidade

MACHITIDWE A ATUMWI 8

18 Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati, 19 "Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera."

20 Petro anayankha kuti, "Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama! 21 Ulibe gawo kapena mbali pa utumikiwu, chifukwa mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu. 22 Lapa zoyipa zakozi ndipo upemphere kwa Ambuye. Mwina adzakukhululukira maganizo a mu mtima mwako. 23 Pakuti ine ndikuona kuti ndiwe wowawidwa mtima ndiponso kapolo wa tchimo."

24 Ndipo Simoni anayankha, "Mundipempherere kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também