30 Pamenepo Filipo anathamangira ku galeta ndipo anamva munthuyo akuwerenga buku la mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti, "Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazi?"
31 Iye anayankha kuti, "Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?" Ndipo iye anayitana Filipo kuti abwere ndikukhala naye mʼgaleta.
32 Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa:
"Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,
kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,
momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.