Pular para o conteúdo
Publicidade

Atos 8

32 Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa:

"Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,

kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,

momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.

33 Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake.

Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake

poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?"

34 Ndunayo inamufunsa Filipo kuti, "Chonde, uzeni, kodi mneneri akuyankhula za ndani, za iye mwini kapena za munthu wina?" 35 Pamenepo Filipo anayambira pa malemba omwewo kumuwuza za Uthenga Wabwino wa Yesu.

Veja também