5 Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko. 6 Gulu la anthu litamva Filipo akulalikira komanso kuona zizindikiro zozizwitsa zimene ankazichita, onse anamvetsetsa zimene iye amanena. 7 Mizimu yoyipa inatuluka mwa anthu ambiri ikufuwula kwambiri ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo ndi olumala anachiritsidwa. 8 Kotero munali chimwemwe chachikulu mu mzindawo.
Publicidade