Maphunziro a Danieli ku Babuloni
1 Chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inabwera ndi kuzinga mzinda wa Yerusalemu ndi kuwuthira nkhondo. 2 Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda mʼdzanja lake, pamodzi ndi zina mwa zida zotumikira mʼNyumba ya Mulungu. Iye anazitenga napita nazo ku nyumba ya mulungu wake ku Babuloni ndi kuziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha mulungu wake.
3 Tsono mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zake kuti abwere nawo ena mwa Aisraeli ochokera mʼbanja laufumu ndi la olemekezeka, 4 achinyamata wopanda chilema, okongola, aluso mu nzeru zonse, okhala ndi chidziwitso, achangu pophunzira, odziwa kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Ndipo anati awaphunzitsenso kuwerenga chiyankhulo cha Ababuloni. 5 Ndipo mfumu imawapatsa tsiku ndi tsiku gawo la chakudya ndi vinyo wa ku nyumba yaufumu, ndi kuti awaphunzitse kwa zaka zitatu, ndipo kenaka adzayambe kutumikira mfumu.
6 Pakati pa amenewa panali ena ochokera ku Yuda: Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya.