17 Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.
18 Ndipo kumapeto kwa masiku amene mfumu inayika kuti adzaonetse anyamatawa ku nyumba yake, mkulu wa nduna za mfumu uja anawapereka iwo kwa Nebukadinezara. 19 Mfumu inayankhula nawo, ndipo panalibe wofanana ndi Danieli; Hananiya Misaeli ndi Azariya; Choncho analowa ndi kukhala otumikira mfumu.