9 "Ine ndikuyangʼanabe ndinaona
"mipando yaufumu ikukhazikitsidwa,
ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake.
Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana;
tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje.
Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto,
ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto.