Pular para o conteúdo
Publicidade

Danieli 9:20-23

Zaka 70

20 Ndikuyankhula ndi kupemphera, kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu anga Aisraeli ndi kupempherera phiri lake loyera kwa Yehova Mulungu wanga, 21 Gabrieli, munthu uja amene ndinamuona mʼmasomphenya poyambirira, anabwera kwa ine mowuluka. Iyi inali nthawi ya nsembe ya madzulo. 22 Anandilangiza kuti, "Danieli ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru kuti uzitha kumvetsa zinthu. 23 Utangoyamba kupemphera, Mulungu anayankha. Tsono ine ndabwera kudzakuwuza yankholo, popeza ndiwe wokondedwa kwambiri. Choncho mvetsetsa pamene ndikufotokoza za zinthu zimene unaziona mʼmasomphenya.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.