Kupembedza Milungu Ina
1 Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, 2 chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, "Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze," (kunena milungu imene simunayidziwe), 3 musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.