Makhalidwe Oletsedwa
9 Mukafika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musakaphunzire makhalidwe onyansa a anthu a mʼdzikolo. 10 Pasapezeke pakati panu munthu wootcha pa moto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe. Asapezekenso pakati panu munthu wowombeza kapena wochita mawula, wolosera, wochita za ufiti, 11 wolodza, kapena woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndi kumafunsira nzeru kwa anthu akufawo. 12 Aliyense wochita zinthu zotere ndi wonyansa pamaso pa Yehova, ndipo chifukwa cha zonyansa zimenezi Yehova adzakupirikitsirani mitundu ya anthu imeneyi.