Mwana Wamwamuna Wowukira
18 Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wowukira amene samvera a abambo ake ndi amayi ake akamuweruza, 19 abambo ndi amayi ake amugwire ndi kupita naye kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda wake ndipo 20 akawawuze akuluakuluwo kuti, "Mwana wathu wamwamunayu ndi wosamva ndi wowukira. Iyeyu satimvera. Ndi mwana wadyera komanso ndi chidakwa." 21 Pamenepo anthu onse a mu mzinda wake adzamuphe ndi miyala. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu. Aisraeli onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha.