Malamulo a Ukwati
13 Ngati munthu akwatira mkazi, ndipo atagona naye nʼkusamufunanso 14 namunyoza ndi kumuyipitsira dzina nʼkumati, "Ine ndinakwatira mkazi uyu, koma pamene ndinakhala naye, sindinachione chizindikiro cha unamwali wake," 15 zikatero abambo ndi amayi ake ayenera kubweretsa chitsimikizo chakuti anali namwali kwa akuluakulu a mzinda ku chipata. 16 Abambo ake a mtsikanayo adzanene kwa akuluakuluwo kuti, "Ine ndinamupatsa munthu uyu mwana wanga wamkazi kuti amukwatire, koma sakumufunanso. 17 Tsopano wamunyoza ndipo wanena kuti, ‘Ine sindinapeze kuti mwana wanu wamkaziyu ndi namwali.’ Koma tsopano onani chitsimikizo ichi cha unamwali wa mwana wanga wamkazi." Kenaka makolo a mtsikanayo adzaonetse kansalu kwa akuluakulu aja,