5 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. 6 Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. 7 Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. 8 Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. 9 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.
Publicidade