16 Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake, 17 kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi 18 kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. 19 Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.