25 Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo 26 kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake. 27 Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro. 28 Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. 29 Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake