21 Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, "Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska. 22 Mutengenso nthambi ya chitsamba cha hisope, muchiviyike mʼmagazi amene mwawayika mʼbeseni ndipo muwaze ena mwa magaziwo pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko. Palibe aliyense wa inu amene adzatuluke mʼnyumba yake mpaka mmawa. 23 Pamene Yehova adzadutsa mʼdziko kudzakantha Aigupto, nʼkuona magazi pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko, Iye adzadutsa khomo limenelo ndipo sadzalola woonongayo kuti alowe mʼnyumba zanu kuti akukantheni.