Pular para o conteúdo
Publicidade

Êxodo 16

11 Yehova anati kwa Mose, 12 "Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ "

13 Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo. 14 Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale. 15 Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, "Kodi timeneti nʼchiyani?" Popeza sanatidziwe.

Mose anawawuza kuti, "Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye.

Veja também