17 Mpongozi wa Mose anayankha kuti, "Zimene mukuchitazi si zabwino. 18 Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. 19 Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. 20 Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. 21 Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. 22 Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. 23 Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere."