Pular para o conteúdo
Publicidade

EKSODO 2

Kubadwa kwa Mose

1 Ndipo munthu wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi wa fuko lomwelo. 2 Mkaziyo anatenga pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo anali wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu. 3 Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo. 4 Mlongo wake wa mwanayo anayima pataliko kuti aone chimene chidzamuchitikira mwanayo.

5 Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge. 6 Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, "Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri."

7 Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, "Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?"

8 Iye anayankha kuti, "Inde, pita." Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo. 9 Mwana wa Farao anati, "Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani." Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera. 10 Mwanayo atakula anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anakhala mwana wake. Iye anamutcha dzina lake Mose, popeza anati, "Ndinamuvuwula mʼmadzi."

Veja também