Pular para o conteúdo
Publicidade

EKSODO 2

5 Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge. 6 Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, "Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri."

7 Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, "Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?"

8 Iye anayankha kuti, "Inde, pita." Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo. 9 Mwana wa Farao anati, "Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani." Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera.

Veja também