Pular para o conteúdo
Publicidade

Eksodo 27:1-8

Guwa Lansembe Yopsereza

1 "Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229. 2 Upange nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo kuti nyangazo ndi guwalo zikhale chinthu chimodzi, ndipo ulikute guwalo ndi mkuwa. 3 Upange ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika yochotsera phulusa, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto. 4 Upange sefa yachitsulo chamkuwa ndipo mʼngodya zake zinayizo upangiremo mphete zamkuwa. 5 Uyike sefayo mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, ndipo ilekezere pakati pa guwa lansembelo. 6 Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndipo uzikutire ndi mkuwa. 7 Pamene mukunyamula guwalo, muzilowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo. 8 Guwalo likhale lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. Ulipange monga momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.