Guwa Lansembe Yofukiza
1 Upange guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. 6 Uyike guwalo patsogolo pa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano. Apa ndi pamene ndizidzakumana nawe.
7 "Aaroni ayenera kumafukiza lubani wonunkhira pa guwalo mmawa uliwonse. Pamene akukonza nyale zija afukizenso lubani. 8 Aaroni ayenera kufukizanso lubani pamene ayatsa nyale madzulo kuti lubani akhale akuyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova kwa mibado imene ikubwera. 10 Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova."