Bezaleli ndi Oholiabu
1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 2 "Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda. 3 Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: 4 Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, 5 kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja.