Pular para o conteúdo
Publicidade

Eksodo 31:1-6

Bezaleli ndi Oholiabu

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 2 "Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda. 3 Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: 4 Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, 5 kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. 6 Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi:

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.