11 Koma Mose anapempha chifundo cha Mulungu wake ndipo anati, "Chonde Yehova, chifukwa chiyani mwakwiyira anthu awa amene munawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu. 12 Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu. 13 Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ " 14 Choncho Yehova analeka ndipo sanawachitire choyipa anthu ake monga anaopsezera.