5 ndipo anati kwa Mose, "Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike."
6 Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, "Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika." Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, 7 chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse.