11 Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. 12 Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo.
Publicidade