Kuthamanga Mpaka Kumapeto pa Mpikisano wa Liwiro
12 Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiyitanira. 13 Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. 14 Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.
Kutsanzira Paulo
15 Choncho ife tonse amene tili okhwima pa moyo wauzimu, tikhale ndi maganizo omwewa. Ndipo ngati pena ndi pena muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa, pameneponso Mulungu adzakuwunikirani.