24 Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo. 25 Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu.
Publicidade
Publicidade