27 Pakuti kwalembedwa kuti,
"Sangalala, iwe mayi wosabala,
amene sunabalepo mwana;
imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe,
iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;
chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri
kuposa mkazi wokwatiwa."
28 Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake. 29 Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero.