16 Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo.
22 Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, 23 kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi. 24 Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo.