5 Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. 6 Yehova anati, "Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. 7 Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane."
8 Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. 9 Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.