Mulungu Ayitana Abramu
1 Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, "Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.
2 "Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu
ndipo ndidzakudalitsa;
ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti
udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.
3 Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe,
ndi kutemberera amene adzatemberera iwe;
ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi
adzadalitsika kudzera mwa iwe."