6 Abramu anati, "Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera." Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa.
7 Mngelo wa Yehova anamupeza Hagara pafupi ndi chitsime mʼchipululu. Chinali chitsime chimene chili mʼmphepete mwa msewu wopita ku Suri. 8 Ndipo mngeloyo anati, "Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?"
Iye anayankha, "Ndikuthawa mbuye wanga Sarai."