10 Tsono mmodzi mwa iwo anati, "Mosakayikira ndidzabweranso pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna."
Koma Sara amene anali kumbuyo kwa Abrahamu pa khoma la tenti ankamva zonsezi. 11 Abrahamu ndi Sara anali okalamba kale ndipo anali ndi zaka zambiri. Sara nʼkuti atapyola kale pa msinkhu oti nʼkubereka. 12 Choncho anangoseka nati mu mtima mwake, "Kodi munthu wothayitha ngati ine ndingasangalalenso kugona pamodzi ndi mbuye wanga? Mwamuna wanga nayenso ndi wokalamba."