21 Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. 22 Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye.
23 Munthu uja anati,
"Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga
ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga;
adzatchedwa ‘mkazi,’
popeza wachokera mwa mwamuna."