15 Madzi atatha mʼbotolo muja, anamuyika mnyamatayo pansi pa zitsamba. 16 Kenaka Hagara anachoka nakakhala pansi cha pakatalipo, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi, popeza mʼmaganizo mwake amati, "Sindingaonerere mwanayu akufa." Ndipo anakhala pansi cha poteropo nʼkumalira.