Pular para o conteúdo
Publicidade

GENESIS 26

Isake ndi Abimeleki

1 Tsono kunagwa njala ina mʼdzikomo kuwonjezera pa ija ya poyamba ya nthawi ya Abrahamu ndipo Isake anapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. 2 Yehova anadza kwa Isake nati, "Usapite ku Igupto; koma ukhale mʼdziko limene ndidzakuwuza kuti ukakhalemo. 3 Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako. 4 Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako, 5 chifukwa Abrahamu anandimvera, nasunga malamulo anga onse." 6 Choncho Isake anakhala ku Gerari.

7 Anthu akumaloko atafunsa Isake za mkazi wake, iye anati, "Ndi mlongo wanga ameneyu." Iye anaopa kunena kuti, "Ndi mkazi wanga ameneyu," popeza ankaganiza kuti anthu akumeneku akhoza kumupha ndi kukwatira mkazi wake popeza Rebeka anali wokongola.

8 Isake atakhalako kumeneko nthawi yayitali, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anasuzumira pa zenera kuyangʼana kunja, ndipo anaona Isake akugwiragwira Rebeka, mkazi wake.

Veja também