Pular para o conteúdo
Publicidade

GENESIS 27

Yakobo Athawira kwa Labani

41 Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, "Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo."

42 Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, "Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire. 43 Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani. 44 Ukakhale naye kwa kanthawi mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utatsika. 45 Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?"

Veja também