17 Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, "Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’
"Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe,
movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo
masiku onse a moyo wako.
18 Mʼnthakamo mudzamera minga ndi nthula
ndipo udzadya zomera zakuthengo.
19 Kuti upeze chakudya udzayenera
kukhetsa thukuta,
mpaka utabwerera ku nthaka
pakuti unachokera kumeneko;
pakuti ndiwe fumbi
ku fumbi komweko udzabwerera."