Pular para o conteúdo
Publicidade

Genesis 45:1,4,5,15

Yosefe Adziwulula kwa Abale Ake

1 Tsono Yosefe sanathenso kuwugwira mtima kuti asalire pamaso pa antchito ake ndipo anafuwula kuti, "Aliyense achoke pamaso panga!" Motero panalibe wina aliyense pamene Yosefe anadziwulula kwa abale ake.

4 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, "Senderani pafupi nane." Atasendera iye anati, "Ine ndine mʼbale wanu Yosefe amene munamugulitsa ku Igupto! 5 Ndipo tsopano, musawawidwe mtima kapena kudzipsera mtima chifukwa choti munandigulitsa ine kuno, popeza Mulungu ananditsogoza ine kuti adzapulumutse miyoyo yanu.

15 Atatero, Yosefe anapsompsona abale ake onse aja, akulira. Pambuyo pake abale ake aja anacheza ndi Yosefe.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.