Pular para o conteúdo
Publicidade

AHEBRI 12

Mulungu Amalanga Ana ake

5 Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa:

"Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye

ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.

6 Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda

ndipo amalanga aliyense amene amamulandira."

7 Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? 8 Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. 9 Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo?

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também