Za Melikizedeki Mkulu wa Ansembe
1 Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. 2 Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, "Mfumu ya chilungamo," kenakanso, "Mfumu ya Salemu," kutanthauza, "Mfumu ya mtendere." 3 Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.