Pular para o conteúdo
Publicidade

Hebreus 8

6 Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.

7 Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. 8 Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati,

"Masiku akubwera," akutero Yehova,

"pamene ndidzachita pangano latsopano

ndi Aisraeli

ndiponso nyumba ya Yuda.

9 Silidzakhala ngati pangano

limene ndinachita ndi makolo awo,

pamene ndinawagwira padzanja

nʼkuwatulutsa ku Igupto

chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija

ndipo Ine sindinawasamalire,

akutero Ambuye.

10 Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli:

Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye,

Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo,

ndi kulemba mʼmitima mwawo.

Ine ndidzakhala Mulungu wawo,

ndipo iwo adzakhala anthu anga.

11 Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake,

kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye

chifukwa onse adzandidziwa,

kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.

12 Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo,

ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo."

13 Ponena kuti, pangano "latsopano" Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.

Veja também