16 Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi, 17 chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo. 18 Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi. 19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse. 20 Iye anati, "Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge."
Publicidade
Publicidade