Dandawulo la Habakuku
2 Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani,
koma wosayankha?
Kapena kufuwulira kwa inu kuti, "Chiwawa kuno!"
koma wosatipulumutsa?
3 Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa?
Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa?
Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa;
pali ndewu ndi kukangana kwambiri.