Pemphero la Yona
1 Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake. 2 Iye anati:
"Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova,
ndipo Iye anandiyankha.
Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo,
ndipo Inu munamva kulira kwanga.