6 Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri;
mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha.
Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo,
Inu Yehova Mulungu wanga.
7 "Pamene moyo wanga umachoka mwa ine,
ine ndinakumbukira Inu Yehova,
ndipo pemphero langa linafika kwa inu,
ku Nyumba yanu yopatulika.