Pular para o conteúdo
Publicidade

YOHANE 1

45 Filipo anakapeza Natanieli ndipo anamuwuza kuti, "Ife tapeza amene Mose analemba za Iye mʼmalamulo, ndi zimene aneneri analembanso za Iye, Yesu wa ku Nazareti, mwana wa Yosefe."

46 Natanieli anafunsa kuti, "Nazareti! Kodi kanthu kalikonse kabwino kangachokere kumeneko?"

Filipo anati, "Bwera udzaone."

47 Yesu atamuona Natanieli akuyandikira, anati kwa iye, "Uyu ndi Mwisraeli weniweni, mwa iye mulibe chinyengo."

48 Natanieli anafunsa kuti, "Kodi mwandidziwa bwanji?"

Yesu anayankha kuti, "Ine ndinakuona iwe utakhala pansi pamtengo wamkuyu Filipo asanakuyitane."

49 Kenaka Natanieli ananena kuti, "Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu; Inu ndinu Mfumu ya Israeli."

50 Yesu anati, "Ukukhulupirira chifukwa chakuti ndakuwuza kuti Ine ndinakuona iwe uli pansi pamtengo wamkuyu? Iwe udzaona zinthu zazikulu kuposa izo." 51 Ndipo Iye anapitirira kuti, "Zoonadi, Ine ndikuwuza kuti iwe udzaona kumwamba, kutatsekuka ndi angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu."

Veja também